11 Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usacimwenso.
12 Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.
13 Cifukwa cace Afarisi anati kwa iye, Mucita umboni wa Inu nokha; umboni wanu suli woona.
14 Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndicita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; cifukwa ndidziwa kumene ndinacokera ndi kumene ndimukako; koma e inu, simudziwa kumene ndicokera, ndi kumene ndimukako.
15 Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu.
16 Ndipo ngati ndiweruza Ine, ciweruziro canga ciri coona; pakuti sindiri pa ndekha, koma ine ndi Atate amene anandituma Ine.
17 Inde kudalembedwa m'cilamulo canu kuti umboni wa anthu awiri uli woona.