16 Ndipo ngati ndiweruza Ine, ciweruziro canga ciri coona; pakuti sindiri pa ndekha, koma ine ndi Atate amene anandituma Ine.
17 Inde kudalembedwa m'cilamulo canu kuti umboni wa anthu awiri uli woona.
18 Ine ndine wakucita umboni wa Ine ndekha, ndipo Atate amene anandituma Ine, acita umboni wa Ine.
19 Cifukwa cace ananena ndi iye, Ali kuti Atate, wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukada-dziwanso Atate wanga.
20 Mau awa analankhula m'nyumba ya cuma ca Mulungu pophunzitsa m'Kacisi; ndipo palibe munthu anamgwira iye, pakuti nthawi yace siinafike.
21 Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'cimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.
22 Cifukwa cace Ayuda ananena, Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, Kumene ndimukako Ine, simudziwa inu kudza?