7 Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda cimo, ayambe kumponya mwala,
8 Ndipo m'mene adaweramanso analemba ndi cala cace pansi.
9 Koma iwo, m'mene adamva, anaturukamo amodzi amodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.
10 Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi?
11 Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usacimwenso.
12 Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.
13 Cifukwa cace Afarisi anati kwa iye, Mucita umboni wa Inu nokha; umboni wanu suli woona.