6 Ndipo anati kwa mfumu, idali yoonadi mbiri ija ndinaimva ine ku dziko langa ya macitidwe anu ndi nzeru zanu.
7 Koma sindinakhulupira mau amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.
8 Odala anthu anu, odala anyamata anu akukhala nthawi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu.
9 Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wacifumu wa Israyeli; popeza Yehova anakonda Israyeli nthawi yosatha, cifukwa cace anakulongani inu ufumu, kuti mucite ciweruzo ndi cilungamo.
10 Ndipo mkaziyo ananinkha mfumu matalenti a golidi zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zaunyinji, ndi timiyala ta mtengo wapatali; sunafikanso unyinji wotero wa zonunkhira wolingana ndi uja mfumu yaikazi inapereka kwa mfumu Solomo.
11 Ndipo zombe za Hiramu zotengera golidi ku Ofiri zinatenganso ku Ofiri mitengo yambiri yambawa, ndi timiyala ta mtengo wapatali.
12 Ndipo mfumu inasema mitengo yambawayo, ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi ya nyumba ya mfumu; ndiponso azeze ndi zisakasa za oyimbawo; siinafika kapena kuonekanso mpaka lero mitengo yotero yambawa.