1 Ndipo mfumu Solomo anakonda akazi ambiri acilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Moabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Zidoni, ndi Ahiti;
2 a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israyeli za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomo anawaumirira kuwakonda.
3 Ndipo anali nao akazi mazana asanu ndi awiri, ana akazi a mafumu, ndi akazi acabe mazana atatu; ndipo akazi ace anapambutsa mtima wace.
4 Ndipo kunali, atakalamba Solomo, akazi ace anapambutsa mtima wace atsate milungu yina; ndipo mtima wace sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wace monga mtima wa Davide atate wace.
5 Tsono Solomo anatsata Asitoreti fano la anthu a Zidoni, ndi Milikomu fano lonyansitsa la Aamoni.
6 Ndipo Solomo anacita coipa pamaso pa Yehova, osatsata Yehova ndi mtima wonse monga Davide atate wace.
7 Pamenepo Salomo anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amoabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, pa phiri liri patsogolo pa Yerusalemu.