6 Ndipo makungubwi anamtengera mkate ndi nyama m'mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje.
7 Ndipo kunacitika, atapita masiku ena mtsinje udaphwa, popeza munalibe mvula m'dziko.
8 Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,
9 Nyamuka, pita ku Zarefati wa ku Zidoni, nukhale kumeneko; taona, ndamlamulira mkazi wamasiye wa kumeneko akudyetse.
10 Tsono iye ananyamuka namka ku Zarefati, nafika ku cipata ca mudzi; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang'ono m'cikho, ndimwe.
11 Ndipo m'mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m'dzanja lako.
12 Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndiribe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndirikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire odekha ndi mwana wanga, tidye, tife.