14 Ndipo anawatuma ku Lebano mwezi umodzi zikwi khumi kuwasintha, mwezi umodzi iwo anali ku Lebano, miyezi iwiri anali kwao; ndipo Adoniramu anali kapitao wa athangata.
15 Ndipo Solomo anawasenzetsa akatundu anthu zikwi makumi asanu ndi awiri, ndi anthu zikwi makumi asanu ndi atatu anatema m'mapiri;
16 osawerenga akapitao a Solomo akuyang'anira nchito, ndiwo zikwi zitatu mphambu mazana atatu, amenewo analamulira anthu aja akugwira nchito.
17 Ndipo mfumu inalamula iwo, natuta miyala yaikuru-ikuru ya mtengo wapatali, kuika maziko ace a nyumbayo ndi miyala yosemasema.
18 Ndipo omanga nyumba a Solomo ndi omanga nyumba a Hiramu ndi anthu a ku Gebala anaisema, naikonza mitengo ndi miyala yakumangira nyumbayo.