8 Ndipo mphikozo zinatalika kuti nsonga za mphiko zidaoneka ku malo opatulika cakuno ca monenera; koma sizinaoneka kubwalo; ndipo zikhala pomwepo mpaka lero lino.
9 Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja amwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israyeli, poturuka iwo m'dziko la Aigupto.
10 Ndipo kunacitika ataturuka ansembe m'malo opatulika, mtambo unadzaza nyumba ya Yehova,
11 ndipo ansembe sanakhoza kuimirira kurumikira cifukwa ca mtambowo, popeza ulemerero wa Yehova unadzazanyumba ya Yehova.
12 Pamenepo Solomo anati, Yehova ananena kuti adzakhala m'mdima waukuru.
13 Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo inu nthawi zosatha.
14 Ndipo mfumu inapotoloka nkhope yace, nidalitsa msonkhano wonse wa Israyeli, Ndi msonkhano wonse wa Israyeli unaimirira.