22 Nati iye, Pamene mwanayo akali ndi moyo, ndinasala kudya ndi kulira, pakuti ndinati, Adziwa ndani kapena Yehova adzandicitira cifundo kuti mwanayo akhale ndi moyo.
23 Koma tsopano wafa, ndidzasaliranjinso kudya? Kodi ndikhoza kumbweza? Ine ndidzamuka kuli iye, koma iye sadzabweranso kwa ine.
24 Ndipo Davide anasangalatsa Bateseba mkazi wace, nalowa kwa iye, nagona naye; ndipo anabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Solomo. Ndipo Yehova anamkonda iye,
25 natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namucha dzina lace Wokondedwa ndi Yehova, cifukwa ca Yehova.
26 Ndipo Yoabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mudzi wacifumu.
27 Yoabu natumiza mithenga kwa Davide nati, Ndaponyana ndi Raba, inde ndalanda mudzi wa pamadzi.
28 Cifukwa cace tsono musonkhanitseanthu otsalawo, nimumangire mudziwo zithando, muulande; kuti ine ndingalande mudziwo, ndipo ungachedwe ndi dzina langa.