16 Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wace m'dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kuticotsa ku colowa ca Mulungu.
17 Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.
18 Pamenepo mfumu inayankha, ninena naye mkaziyo, Usandibisire kanthu ka zimene ndidzakufunsa iwe. Mkaziyo nati, Mbuye wanga mfumu anene.
19 Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yoabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yoabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu.
20 Mnyamata wanu Yoabu anacita cinthu ici kuti asandulize mamvekedwe a mranduwo. Ndipo mbuye wanga ali wanzeru, monga ndi nzeru ya mthenga wa Mulungu, kudziwa zonse ziri m'dziko lapansi.
21 Ndipo mfumuyo inanena ndi Yoabu, Taonatu, ndacita cinthu ici; cifukwa cace, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu.
22 Ndipo Yoabu anagwa nkhope yace pansi, namlambira, nadalitsa mfumuyo; nati Yoabu, Lero mnyamata wanu ndadziwa kuti munandikomera mtima, mbuye wanga mfumu, popeza mfumu yacita copempha mnyamata wace.