26 Ndipo pometa tsitsi lace amameta potsiriza caka, cifukwa tsitsi linamlemerera, cifukwa cace atalimeta anayesa tsitsi la pa mutu wace, napeza masekeli mazana awiri, monga mwa muyeso wa mfumu.
27 Ndipo kwa Abisalomu kunabadwa ana amuna atatu ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lace ndiye Tamara, iye ndiye mkazi wokongola nkhope.
28 Ndipo Abisalomu anakhala ku Yerusalemu zaka ziwiri zathunthu, osaona nkhope ya mfumu.
29 Pamenepo Abisalomu anaitana Yoabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yaciwiri, koma anakana kubwera.
30 Cifukwa cace iye anati kwa anyamata ace, Onani munda wa Yoabu uli pafupi ndi wanga, ndipo iye ali ndi barele pamenepo, mukani mukamtenthere. Ndipo anyamata a Abisalomu anatentha za m'mundawo.
31 Pamenepo Yoabu ananyamuka nafika kwa Abisalomu ku nyumba yace, nanena naye, Cifukwa ninji anyamata anu anatentha za m'munda mwanga;
32 Abisalomu nayankha Yoabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kucokera ku Gesuri? mwenzi nditakhala komweko; cifukwa cace tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu.