4 Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse ziri zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.
5 Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panaturuka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Sauli, dzina lace ndiye Simeyi, mwana wa Gera; iyeyu anaturukako, nayenda natukwana.
6 Ndipo iye anaponya miyala Davide ndi anyamata onse a mfumu Davide, angakhale anthu onse ndi ngwazi zonse zinali kudzanja lamanja ndi ku dzanja lamanzere kwace.
7 Ndipo anatero Simeyi pakutukwana, Coka, coka, munthu wa mwazi iwe, woipa iwe;
8 Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Sauli, amene iwe wakhala mfumu m'malo mwace; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m'dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m'kuipa kwako kwa iwe wekha, cifukwa uli munthu wa mwazi.
9 Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Garu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wace.
10 Mfumu niti, Ndiri ndi ciani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero cifukwa ninji?