6 Ndipo iye anaponya miyala Davide ndi anyamata onse a mfumu Davide, angakhale anthu onse ndi ngwazi zonse zinali kudzanja lamanja ndi ku dzanja lamanzere kwace.
7 Ndipo anatero Simeyi pakutukwana, Coka, coka, munthu wa mwazi iwe, woipa iwe;
8 Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Sauli, amene iwe wakhala mfumu m'malo mwace; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m'dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m'kuipa kwako kwa iwe wekha, cifukwa uli munthu wa mwazi.
9 Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Garu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wace.
10 Mfumu niti, Ndiri ndi ciani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero cifukwa ninji?
11 Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ace onse, Onani, mwana wanga woturuka m'matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza.
12 Kapena Yehova adzayang'anira cosayeneraci alikundicitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera cabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero.