26 Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira buru kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndiri wopunduka.
27 Ndipo iye anandinamizira mnyamata wanu kwa mbuye wanga mfumu; koma mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Yehova; cifukwa cace citani cimene cikukomerani.
28 Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjeze kudandaulira kwa mfumu?
29 Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo.
30 Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere ku nyumba yace.
31 Ndipo Barizilai, Mgileadi anatsika kucokera ku Rogelimu; nayambuka pa Yordano ndi mfumu, kuti akamuolotse pa Yordano.
32 Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka cakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.