16 Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzace, nagwaza ndi lupanga lace m'nthiti mwa mnzaceo Comweco anagwa limodzi; cifukwa cace malo aja anachedwa Dera la Mipeni la ku Gibeoni.
17 Ndipo tsikulo nkhondo inakula ndithu. Ndi Abineri ndi anthu a Israyeli anathawa pamaso pa anyamata a Davide.
18 Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yoabu, Abisai ndi Asaheli. Ndipo Asaheli anali waliwiro ngati nyama ya kuthengo.
19 Ndipo Asaheli anapitikitsa Abineri. Ndipo m'kuthamanga kwace sanapambukira kulamanja, kapena kulamanzere, pakutsata Abineri.
20 Pomwepo Abineri anaceuka nati, Kodi ndi iwe Asaheli? iye nayankha, Ndine.
21 Ndipo Abineri ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zace. Koma Asaheli anakana kupambuka pakumtsata iye.
22 Ndipo Abineri anabwereza kunena kwa Asaheli, Pambuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yoabu?