2 Ndipo mfumu inaitana Agibeoni, ninena nao (koma Agibeoni sanali a ana a Israyeli, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israyeli anawalumbirira kwa iwo, koma Sauli anafuna kuwapha mwa cangu cace ca kwa ana a Israyeli ndi a Yuda).
3 Ndipo Davide ananena ndi Agibeoni, Ndidzakucitirani ciani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi ciani kuti mukadalitse colowa ca Yehova?
4 Ndipo Agibeoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golidi wa Sauli kapena nyumba yace; ndiponso sitifuna kupha munthu ali yense wa m'Israyeli. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakucitirani.
5 Ndipo anati kwa mfumu, Munthu uja anatitha natilingalira pa ife cotionongera kuti tisakhalenso m'malire ali onse a Israyeli,
6 mutipatse ana ace amuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapacika kwa Yehova m'Gibeya wa Sauli, wosankhika wa Yehova, Mfumu niti, Ndidzawapereka.
7 Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Jonatani, mwana wa Sauli, cifukwa ca lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Jonatani mwana wa Sauli.
8 Koma mfumu inatenga ana amuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Sauli, ndiwo Arimoni ndi, Mefiboseti; ndiponso ana amuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Sauli, amene iye anambalira Adriyeli mwana wa Barizilai Mmeholati;