11 monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israyeli; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.
12 Pamene masiku ako akadzakwaniridwa, ndipo iwe udzagona ndi makolo ako, Ine ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, imene idzaturuka m'matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace.
13 Iye adzamangira dzina langa nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa cimpando ca ufumu wace ku nthawi zonse.
14 Ndidzakhala atate wace, iye nadzakhala mwana wanga; akacita coipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;
15 koma cifundo canga sicidzamcokera iye, monga ndinacicotsera Sauli amene ndinamcotsa pamaso pako.
16 Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wacifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.
17 Monga mwa mau onse awa ndi monga mwa masomphenya onse awa, momwemo Natani analankhula ndi Davide.