1 AWA ndi mau amene Mose ananena kwa Israyeli wonse, tsidya la Yordano m'cipululu, m'cidikha ca pandunji pa Sufu, pakati pa Parani, ndi Tofeli, ndi Labani, ndi Hazeroti, ndi Di Zahabi.
2 Ulendo wace wocokera ku Horebe wofikira ku Kadesi Barinea, wodzera njira ya phiri la Seiri, ndiwo wa masiku khumi ndi limodzi.
3 Ndipo kunali, caka ca makumi anai, mwezi wakhumi ndi umodzi, tsiku loyamba la mweziwo, Mose ananena ndi ana a Israyeli, monga mwa zonse Yehova adamlamulira awauze;
4 atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basana, wakukhala m'Asitaroti, ku Edrei.
5 Tsidya lija la Yordano, m'dziko la Moabu, Mose anayamba kufotokozera cilamulo ici, ndi kuti.