1 Masiku aja Yehova anati kwa ine, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja, nukwere kuno kwa Ine m'phiriumu, nudzipangire likasa lamtengo.
2 Ndipo ndidzalembera pa magomewo mauwo anali pa magome oyamba aja amene unawaswa, ndipo uwaike m'likasamo.
3 Potero ndinapanga likasa la mtengo wasitimu, ndinasemanso magome awiri amiyala onga oyamba aja, ndi kukwera m'phirimo, magome awiri ali m'manja mwanga.
4 Ndipo analembera pamagome, monga mwa malembedwe oyamba, mau khumiwo, amene Yehova adanena ndi inu m'phirimo, ali pakati pa moto, tsiku la kusonkhanako; ndipo Yehova anandipatsa awa.
5 Ndipo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi kuika magome m'likasa ndinalipanga, ali m'menemo monga Yehova anandilamulira ine.