22 Muzipereka ndithu limodzi la magawo khumi la zipatso zonse za mbeu zanu, zofuma kumunda, caka ndi caka.
23 Ndipo muzidye pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo m'mene asankhamo iye, kukhalitsamo dzina lace; limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, la vinyo wanu, ndi la mafuta anu, ndi oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi a nkhosa ndi mbuzi zanu; kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.
24 Ndipo ikakutalikirani njira kotero kuti simukhoza kulinyamula, popeza malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, kuikapo dzina lace, akutanimphirani; atakudalitsani Yehova Mulungu wanu;
25 pamenepo mulisinthe ndarama, ndi kumanga ndarama ikhale m'dzanja mwanu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;
26 ndipo mugule ndi ndaramazo ciri conse moyo wanu ukhumba, ng'ombe kapena nkhosa, kapena vinyo, kapena cakumwa colimba, kapena ciri conse moyo wanu ukufunsani; nimudye pomwepo pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera, inu ndi a pabanja panu.
27 Koma Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, musamamtaya, popeza alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi inu.
28 Pakutha pace pa zaka zitatu muziturutsa magawo onse a magawo khumi a zipatso zanu za caka ico, ndi kuwalinditsa m'mudzi mwanu;