17 apereke yense monga mwa mphatso ya m'dzanja lace, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani.
18 Mudziikire oweruza ndi akapitao m'inidzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mapfuko anu; ndipo aweruze anthu ndi ciweruzo colungama.
19 Musamapotoza ciweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira cokometsera mlandu; popeza cokometsera mlandu cidetsa maso a anzeru, niciipsa mau a olungama.
20 Cilungamo, cilungamo ndico muzicitsata, kuti mukhale ndi moyo ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.
21 Musamadziokera mitengo iri yonse ikhale nkhalango pafupi pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, limene mwadzimangira.
22 Ndipo musamadziutsira coimiritsa ciri conse cimene Yehova Mulungu wanu adana naco.