1 Ansembe Alevi, pfuko lonse la Levi, alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi Israyeli; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi colowa cace,
2 Alibe colowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wace ndiye colowa cao, monga ananena nao.
3 Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng'ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m'masaya ndi chipfu.
4 Zipatso zoyamba za tirigu wanu, za vinyo wanu, ndi za mafuta anu ndi ubweya woyamba kuusenga, muwapatse izi.