22 monga iye anacitira ana a Bsau, akukhala m'Seiri, pamene anaononga Ahori pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao kufikira lero lomwe.
23 Kunena za Aavi akukhala m'midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m'malo mwao.)
24 Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, M-amori, ndi dziko lace m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.
25 Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kucititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa cifukwa ca iwe.
26 Ndipo ndinatuma amithenga ocokera ku cipululu ca Kedemoti kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi mau a mtendere, ndi kuti,
27 Ndipitire m'dziko mwako; ndidzatsata mseu, osapatuka ine ku dzanja lamanja kapena kulamanzere,
28 Undigulitse cakudya ndi ndarama, kuti ndidye; ndi kundipatsa madzi kwa ndarama, kuti ndimwe; cokhaci ndipitire coyenda pansi;