1 Pamene muturuka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magareta ndi anthu akucurukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ali ndi inu.
2 Ndipo kudzali, pamene muyandikiza kunkhondo, ayandikize wansembe nanene ndi anthu,
3 nati nao, Tamverani, Israyeli, muyandikiza kunkhondo lero paadani anu; musalumuka mitima yanu; musacita mantha, kapena kunjenjemera, kapena kuopsedwa pamaso pao;
4 pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye wakumuka nanu, kugwirira inu pa adani anu, kukupulumutsani.
5 Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? amuke nabwerere kunyumba kwace, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina.
6 Ndipo ndani munthuyo ananka munda wamphesa osalawa zipatso zace? amuke nabwerere ku nyumba yace, kuti angafe kunkhondo, nangalawe munthu wina zipatso zace.