4 ndipo akuru a mudzi uwu atsike nao msotiwo ku cigwa coyendako madzi, cosalima ndi cosabzala, naudula khosi msotiwo m'cigwamo;
5 ndipo ansembe, ana a Levi, ayandikize; pakuti Yehova Mulungu wanu anasankha iwo kumtumikira ndi kudalitsa m'dzina la Yehova; ndipo kutengana konse ndi kupandana konse kukonzeke monga mwa mau awa.
6 Ndipo akuru onse a mudziwo wokhala pafupi pa munthu wophedwayo azisamba manja ao pa msoti woudula khosi m'cigwamo;
7 nayankhe nati, Manja athu sanakhetsa mwazi uwu, ndi maso athu sanauona.
8 Landirani, Yehova, cotetezera anthu anu Israyeli, amene munawaombola, ndipo musalole mwazi wosacimwa ukhale pakati pa anthu anu Israyeli; ndipo adzawatetezera ca mwaziwo.
9 Cotero mudzicotsere mwazi wosacimwa pakati panu, pakuti wacita coyenera pamaso pa Yehova.
10 Pamene muturuka kumka ku nkhondo ya pa adani anu, ndipo Yehova Mulungu wanu awapereka m'manja mwanu, ndipo muwagwira akhale akapolo anu;