1 Ndipo kudzali, utakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu, ndipo mwacilandira ndi kukhala m'mwemo;
2 kuti muzitengako zoyamba za zipatso zonse za nthaka, zakubwera nazo inu zocokera m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndi kuziika mumtanga, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lace.
3 Ndipo mufike kwa wansembe wakukhala m'masiku awa, ndi kunena naye, Ndibvomereza lero lino kwa Yehova Mulungu wako, kuti ndalowa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo athu, kuti adzatipatsa ili.
4 Ndipo wansembe alandire mtanga m'manja mwanu, ndi kuuika pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu.