15 Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kucita malamulo ace onse ndi malemba ace amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani,
16 Mudzakhala otembereredwa m'mudzi, ndi otembereredwa pabwalo.
17 Zidzakhala zotembereredwa mtanga wanu ndi coumbiramo mkate wanu.
18 Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.
19 Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa poturuka inu.
20 Yehova adzakutumizirani temberero, cisokonezeko, ndi kudzudzula monsemo mukaturutsa dzanja lanu kucita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatayika rosanga, cifukwa ca zocita inu zoipa, zimene wandisiya nazo,
21 Yehova adzakumamatiritsani mliri kufikira akakuthani kukucotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.