30 Mudzaparana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m'mwemo; mudzanka munda wamphesa, osalawa zipatso zace.
31 Adzapha ng'ombe yanu pamaso panu, osadyako inu; adzalanda buru wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.
32 Adzapereka ana anu amuna ndi akazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu.
33 Mtundu wa anthu umene simudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi nchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;
34 nimudzakhala oyeruka cifukwa comwe muciona ndi maso anu,
35 Yehova adzakukanthani ndi cironda coipa cosacira naco kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pa mutu panu.
36 Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu yina ya mitengo ndi miyala.