33 Mtundu wa anthu umene simudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi nchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;
34 nimudzakhala oyeruka cifukwa comwe muciona ndi maso anu,
35 Yehova adzakukanthani ndi cironda coipa cosacira naco kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pa mutu panu.
36 Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu yina ya mitengo ndi miyala.
37 Ndipo mudzakhala codabwitsa, ndi nkhani, ndi nthanthi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko.
38 Mudzaturuka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha.
39 Mudzanka m'minda yamphesa ndi kuilima, koma osamwa vinyo wace, kapena kuchera mphesa zace, popeza citsenda cidzaidya.