55 osapatsako mmodzi yense wa iwowa nyama ya ana ace alinkudyayo, popeza sikamtsalira kanthu; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu monse.
56 Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lace popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lace lidzamuipira mwamuna wa pamtima pace, ndi mwana wace wamwamuna ndi wamkazi;
57 ndico dfukwa ca matenda akuturuka pakati pa mapazi ace, ndi ana ace adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdaniwanu m'midzi mwanu.
58 Mukapanda kusamalira kucita mau onse a cilamulo ici olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo YEHOVA MULUNGU ANU;
59 Yehova adzacita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwiza, miliri yaikuru ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa.
60 Ndipo adzakubwezerani nthenda zonse za Aigupto, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu.
61 Ndiponso nthenda zonse ndi miliri yonse zosalembedwa m'buku la cilamulo ici, Yehova adzakutengerani izi, kufikira mwaonongeka.