64 Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu yina, imene simunaidziwa, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.
65 Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.
66 Ndipo moyo wanu udzakhala wanjiranjira pamaso panu, ndipo mudzacita mantha usiku ndi usana, osakhazika mtima za moyo wanu.
67 M'mawa mudzati, Mwenzi atafika madzulo! ndi madzulo mudzati, Mwenzi utafika m'mawa! cifukwa ca mantha a m'mtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi cifukwa ca zopenya maso anu zimene mudzazipenya.
68 Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Aigupto ndi ngalawa, pa njira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogulainu.