3 mayesero akuruwa maso anu anawapenya, zizindikilozo, ndi zozizwa zazikuru zija;
4 koma Yehova sanakupatsani mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.
5 Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m'cipululu; zobvala zanu sizinatha pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinatha pa phazi lanu.
6 Simunadya mkate, simunamwa vinyo kapena cakumwa colimba; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
7 Ndipo pamene munafika pamalo pano, Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basana, anaturuka kudzakomana nafe kunkhondo, ndipo tinawakantha;
8 ndipo tinalanda dziko lao, ndi kulipereka likhale colowa cao ca Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la hafu la Manase.
9 Cifukwa cace sungani mau a cipangano ici ndi kuwacita, kuti mucite mwanzeru m'zonse muzicita.