1 Ndipo kudzakhala, zikakugwerani zonsezi, mdalitso ndi temberero, ndinaikazi pamaso panu, ndipo mukazikumbukila mumtima mwanu mwa amitundu onse, amene Yehova Mulungu wanu anakupitikitsiraniko;
2 nimukabwerera kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kumvera mali ace, monga mwa zonse ndikuuzani lero lino, inu ndi ana anu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse;
3 pamenepo Yehova Mulungu wanu adzaucotsa ukapolo wanu, ndi kukucitirani cifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko.
4 Otayika anu akakhala ku malekezero a thambo, Yehova Mulungu wanu adzakumemezani kumeneko, nadzakutenganiko;
5 ndipo Yehova Mulungu wanu adzakulowetsani m'dziko lidakhala lao lao la makolo anu, nilidzakhala lanu lanu; ndipo adzakucitirani zokoma, ndi kukucurukitsani koposa makolo anu.