14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'cihema cokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'cihema cokomanako.
15 Ndipo Yehova anaoneka m'cihema, m'mtambo njo; ndipo mtambo njo unaima pa khomo la cihema.
16 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, oadzatsata ndi cigololo milungu yacilendo ya dziko limene analowa pakati pace, nadzanditava Ine, ndi kutyola cipangano canga ndinapangana naoco.
17 Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zobvuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?
18 Koma Ine ndidzabisatu nkhope yanga tsiku lija cifukwa ca zoipa zonse adazicita; popeza anadzitembenukira milungu yina.
19 Ndipo tsopano mudzilemberere nyimbo iyi, ndi kuphunzitsa ana a Israyeli iyi: mulike m'kamwa mwao, kuti nyimbo iyi indicitire mboni yotsutsa ana a Israyeli.
20 Pakuti nditakalowetsa awa m'dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu yina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kutyola cipangano canga.