20 Pakuti nditakalowetsa awa m'dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu yina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kutyola cipangano canga.
21 Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zobvuta zambiri, nyimbo iyi idzacita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m'kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azicita lero lino, ndisanawalowetse m'dziko limene ndinalumbira.
22 Potero Mose analembera nyimboyi tsiku lomweli, naiphunzitsa ana a Israyeli.
23 Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israyeli m'dziko limene ndinawalumbirira: ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.
24 Ndipo kunali, Mose atatha kulembera mau a cilamulo ici m'buku, kufikira atalembera onse,
25 Mose anauza Alevi akunyamula likasa la cipangano la Yehova, ndi kuti,
26 Landirani buku ili la cilamulo, nimuliike pambali pa likasa la cipangano la Yehova Mulungu wanu, likhale komweko mboni yakutsutsa inu.