22 Potero Mose analembera nyimboyi tsiku lomweli, naiphunzitsa ana a Israyeli.
23 Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israyeli m'dziko limene ndinawalumbirira: ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.
24 Ndipo kunali, Mose atatha kulembera mau a cilamulo ici m'buku, kufikira atalembera onse,
25 Mose anauza Alevi akunyamula likasa la cipangano la Yehova, ndi kuti,
26 Landirani buku ili la cilamulo, nimuliike pambali pa likasa la cipangano la Yehova Mulungu wanu, likhale komweko mboni yakutsutsa inu.
27 Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova: koposa kotani nanga nditamwalira ine!
28 Ndisonkhanitsire akuru onse a mapfuko anu, ndi akapitao anu, kuti ndinene mau awa m'makutu mwao, ndi kucititsa mboni kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse iwo.