26 Landirani buku ili la cilamulo, nimuliike pambali pa likasa la cipangano la Yehova Mulungu wanu, likhale komweko mboni yakutsutsa inu.
27 Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova: koposa kotani nanga nditamwalira ine!
28 Ndisonkhanitsire akuru onse a mapfuko anu, ndi akapitao anu, kuti ndinene mau awa m'makutu mwao, ndi kucititsa mboni kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse iwo.
29 Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo cidzakugwerani coipa masiku otsiriza; popeza mudzacita coipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace ndi nchito za manja anu.
30 Ndipo Mose ananena mau a nyimbo iyi m'makutu mwa msonkhano wonse wa Israyeli, kufikira adatha.