1 Kumwamba kuchere khutu, ndipo ndidzanena;Ndi dziko lapansi limve mau a m'kamwa mwanga;
2 Ciphunzitso canga cikhale ngati mvula;Maneno anga agwe ngati mame;Ngati mvula yowaza pamsipu,Ndi monga madontho a mvula pazitsamba.
3 Pakuti ndidzalalika dzina la Yehova;Nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu.
4 Thanthwe, nchito yace ndi yangwiro;Pakuti njira zace zonse ndi ciweruzo;Mulungu wokhulupirika ndi wopanda cisalungamo;Iye ndiye wolungama ndi wolunjika,