1 Kumwamba kuchere khutu, ndipo ndidzanena;Ndi dziko lapansi limve mau a m'kamwa mwanga;
2 Ciphunzitso canga cikhale ngati mvula;Maneno anga agwe ngati mame;Ngati mvula yowaza pamsipu,Ndi monga madontho a mvula pazitsamba.
3 Pakuti ndidzalalika dzina la Yehova;Nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu.
4 Thanthwe, nchito yace ndi yangwiro;Pakuti njira zace zonse ndi ciweruzo;Mulungu wokhulupirika ndi wopanda cisalungamo;Iye ndiye wolungama ndi wolunjika,
5 Anamcitira zobvunda si ndiwo ana ace, cirema ncao;Iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.
6 Kodi mubwezera Yehova cotero,Anthu inu opusa ndi opanda nzeru?Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuyewanu;Anakulengani, nakukhazikitsani?
7 Kumbukirani masiku akale,Zindikirani zaka za mibadwo yambiri;Funsani atate wanu, adzakufotokozerani;Akuru anu, adzakuuzani.