12 Yehova yekha anamtsogolera,Ndipo palibe mulungu wacilendo naye.
13 Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi,Ndipo anadya zipatso za m'minda;Namyamwitsa uci wa m'thanthwe,Ndi mafutam'mwala wansangalabwe;
14 Mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa,Ndi mafuta a ana a nkhosa,Ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basana, ndi atonde,Ndi imso zonenepa zatirigu;Ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa,
15 Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira;Wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta;Pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga,Napeputsa thanthwe la cipulumutso cace.
16 Anamcititsa nsanje ndi milungu yacilendo,Anautsa mkwiyo wace ndi zonyansa.
17 Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai;Milungu yosadziwa iwo,Yatsopano yofuma pafupi, Imene makolo anu sanaiopa,
18 Mwaleka Thanthwe limene linakubalani,Mwaiwala Mulungu amene anakulengani.