18 Mwaleka Thanthwe limene linakubalani,Mwaiwala Mulungu amene anakulengani.
19 Ndipo Yehova anaciona, nawanyoza,Pakuipidwa nao ana ace amuna, ndi akazi.
20 Ndipo iye anati, Ndidzawabisira nkhope yanga,Ndidzaona kutsiriza kwao;Popeza iwo ndiwo mbadwo wopulukira,Ana osakhulupirika iwo.
21 Anautsa nsanje yanga ndi cinthu cosati Mulungu;Anautsa mkwiyo wanga om zopanda pace zao.Ndidzautsa nsanje yao ndi iwo osakhala mtundu wa anthu;Ndidzautsa mkwiyo wao ndi mtundu wa anthu opusa.
22 Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga,Utentha kumanda kunsiUkutha dziko lapansi ndi zipatso zaceNuyatsa maziko a mapiri,
23 Ndidzawaunjikira zoipa;Ndidzawathera nubvi yanga.
24 Adzaonda nayo njalaAdzanyekeka ndi makala a moto, cionongeko cowawa;Ndipo ndidzawatumizira mana a zirombo,Ndi ululu wa zokwawa m'pfumbi.