3 Pakuti ndidzalalika dzina la Yehova;Nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu.
4 Thanthwe, nchito yace ndi yangwiro;Pakuti njira zace zonse ndi ciweruzo;Mulungu wokhulupirika ndi wopanda cisalungamo;Iye ndiye wolungama ndi wolunjika,
5 Anamcitira zobvunda si ndiwo ana ace, cirema ncao;Iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.
6 Kodi mubwezera Yehova cotero,Anthu inu opusa ndi opanda nzeru?Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuyewanu;Anakulengani, nakukhazikitsani?
7 Kumbukirani masiku akale,Zindikirani zaka za mibadwo yambiri;Funsani atate wanu, adzakufotokozerani;Akuru anu, adzakuuzani.
8 Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu colowacao,Pamene anagawa ana a anthu,Anaika malire a mitundu ya anthu,Monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israyeli,
9 Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ace;Yakobo ndiye muyeso wa colowacace.