41 Ndikanola lupanga langa lonyezimira,Ndi dzanja langa likagwira ciweruzo;Ndidzabwezera cilango ondiukira,Ndi kulanga ondida.
42 Mibvi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi,Ndi lupanga langa lidzalusira nyama;Ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa,Ndi mutu wacitsitsi wa mdani,
43 Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ace;Adzalipsira mwazi wa atumiki ace,Adzabwezera cilango akumuukira,Nadzafafanizira zoipa dziko lace, ndi anthu ace.
44 Ndipo anadza Mose nanena mau onse a nyimbo iyi m'makutu mwa anthu, iye, ndi Hoseya mwana wa Nuni.
45 Ndipo Mose anatha kunena mau awa onse kwa Israyeli wonse;
46 nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikucitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwacita mau onse a cilamulo ici.
47 Pakuti sicikhala kwa inu cinthu copanda pace, popeza ndico moyo wanu, ndipo mwa cinthu ici mudzacurukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordano, kulilandira.