22 Ndi za Dani anati,Dani ndiye mwana wa mkango,Wakutumpha moturuka m'Basana.
23 Za Nafitali anati,Nafitali, wokhuta nazo zomkondweretsa,Wodzala ndi mdalitso wa Yehova;Landira kumadzulo ndi kumwela.
24 Ndi za Aseri anati,Aseri adalitsidwe mwa anawo;Akhale wobvomerezeka mwa abale ace,Abviike phazi lace m'mafuta.
25 Nsapato zako zikhale za citsulo ndi mkuwa;Ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako.
26 Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe,Wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza,Ndi pa mitambo m'ukulu wace.
27 Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako;Ndi pansipo pali manja osatha.Ndipo aingitsa mdani pamaso pako,Nati, Ononga.
28 Ndipo Israyeli akhala mokhazikika pa yekha;Kasupe wa Yakobo;Akhala m'dziko la tirigu ndi vinyo;Inde thambo lace likukha mame.