22 Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau akuru; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.
23 Ndipo kunali, pamene munamva liu loturuka pakati pa mdima, potentha phiri ndi moto, munayandikiza kwa ine, ndiwo mafumu onse a mapfuko anu ndi akuru anu;
24 ndipo munati, Taonani, Yehova Mulungu wathu anationetsa ulemerero wace, ndi ukuru wace, ndipo tidamva liu lace ali pakati pa mote; tapenya lero lino kuti Mulungu anena ndi munthu, ndipo akhala ndi moyo.
25 Ndipo tsopano tiferenji? popeza mote waukuru uwu udzatitha. Tikaonjeza kumva mau a Yehova Mulungu wathu, tidzafa.
26 Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife, nakhala ndi moyo?
27 Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzicita.
28 Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, pamene munanena ndi ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Ndidamva mau a kunena kwao kwa anthu awa, amene ananena ndi iwe; cokoma cokha cokha adanenaci.