16 Musamayesa Yehova Mulungu wanu, monga munamyesa m'Masa.
17 Muzisunga mwacangu malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi mboni zace, ndi malemba ace, amene anakulamulirani.
18 Ndipo muzicita zolunjika ndi zokoma pamaso pa Yehova; kuti cikukomereni, ndi kuti mulowe kukalandira dziko lokomali Yehova analumbirira makolo anu,
19 kuingitsa adani anu onse pamaso panu, monga Yehova adanena.
20 Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Mbonizo, ndi malemba, ndi maweruzo, zimene Yehova Mulungu wathu anakulamulirani, zitani?
21 Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo a Farao m'Aigupto; ndipo Yehova anatiturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu.
22 Ndipo Yehova anapatsa zizindikilo ndi zozizwa zazikuru ndi zowawa m'Aigupto, pa Farao, ndi pa nyumba yace yonse, pamaso pathu;