21 Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo a Farao m'Aigupto; ndipo Yehova anatiturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu.
22 Ndipo Yehova anapatsa zizindikilo ndi zozizwa zazikuru ndi zowawa m'Aigupto, pa Farao, ndi pa nyumba yace yonse, pamaso pathu;
23 ndipo anatiturutsa komweko, kuti atilowetse, kutipatsa dzikoli analumbirira makolo athu.
24 Ndipo Yehova anatilamulira tizicita malemba awa onse, kuopa Yehova Mulungu wathu, kuti tipindule nako masiku onse, kuti atisunge amoyo, monga lero lino.
25 Ndipo kudzakhala kwa ife cilungamo, ngati tisamalira kucita malamulo awa onse pamaso pa Yehova Mulungu wathu, monga anatilamuliraife.