7 ndipo muziwaphunzitsa mwacangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.
8 Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati cizindikilo, ndipo akhale ngati capamphumi pakati pa maso anu.
9 Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu.
10 Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; midzi yaikuru ndi yokoma, imene simunaimanga;
11 ndi nyumba zodzala nazo zokoma ziri zonse, zimene simunazidzaza, ndi zitsime zosema, zimene simunazisema, minda yampesa, ndi minda yaazitona, zimene simunazioka, ndipo mutakadya ndi kukhuta;
12 pamenepo mudzicenjere mungaiwale Yehova, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo,
13 Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzichula dzina lace.