9 Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu.
10 Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; midzi yaikuru ndi yokoma, imene simunaimanga;
11 ndi nyumba zodzala nazo zokoma ziri zonse, zimene simunazidzaza, ndi zitsime zosema, zimene simunazisema, minda yampesa, ndi minda yaazitona, zimene simunazioka, ndipo mutakadya ndi kukhuta;
12 pamenepo mudzicenjere mungaiwale Yehova, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo,
13 Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzichula dzina lace.
14 Musamatsata milungu yina, milungu yina ya mitundu ya anthu akuzinga inu;
15 pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukucotsani pankhope pa dziko lapansi.