1 Muzisamalira kucita malamulo onse amene ndikuuzani lero lino, kuti mukhale ndi moyo, ndi kucuruka, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova analumbirira makolo anu.
2 Ndipo mukumbukile njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'cipululu zaka izi makumi anai, kuti akucepetseni, kukuyesani, kudziwa cokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ace, kapena iai.
3 Ndipo anakucepetsani, nakumvetsani odala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwa, angakhale makolo anu sanawadziwa; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakuturuka m'kamwa mwa Yehova.
4 Zobvala zanu sizinatha pathupi panu, phazi lanu silinatupa zaka izi makumi anai.
5 Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wace, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.